KAFUKUFUKU WA AMP

KODI KAFUKUFUKU WA KATEMERA WA ASILIKALI OTETEZA M’THUPI ndi chiyani?

Mawu akuti AMP ndi achingerezi ndipo amatanthauza Kuteteza Matenda Kudzera mwa Asilikali kapena kuti Antibody Mediated Prevention pa Chingerezi. Iyi ndi njira yopatsira anthu asilikali pofuna kuona ngati angateteze anthuwo ku kachirombo ka HIV.

Kafukufuku wa katemera wa AMP ndi njira yatsopano yotetezera kachirombo ka HIV yomwe ndiyofanana ndi zomwe zakhala zikuchitika mu kafukufuku wa katemera wa HIV. Mukafukufuku woyambilira wa HIV, anthu ankalandira katemera ndipo ofufuza amadikira kuti awone ngati matupi a anthuwo angapange chitetezo chogonjetsa kachirombo ka HIV. M’kafukufuku uno, tidumpha ndondomeko imeneyi, ndipo tipereka mankhwalawa powabayira m’misempha pogwiritsa ntchito njira yodziwika kwambiri yoika dilipi. Uyu ndi kafukufuku woyamba wowona ngati chitetezo cha m’thupi chingathe kuteteza kachirombo ka HIV.

KODI ASILIKALIWA NDI CHIYANI?

Asilikali am’thupi ndi mapoloteni achibadwidwe a m’thupi omwe amalimbana ndi matenda. Mapoloteniwa amatha kumatilira kunja kwa mabakiteliya ndi tizirombo tina pofuna kutilepheletsa kubweretsa matenda m’thupi. Uku kumatchedwa “kufowoketsa.” Mapoloteniwa, omwe amatchedwa VRC01 ndi njira yaikulu yofowoketsera kachirombo ka HIV. Malinga ndi kuwunika kwa mulabu kwasonyeza kuti mapoloteni ofowoketsa HIV monga VRC01 amateteza kutenga mitundu yosiyanasiyana ya kachirombo ka HIV padziko lonse. Izi zimachitika pomatilira kunja kwa kachiromboka m’malo amene HIV imagwiritsa ntchito polimbana ndi maselo athanzi m’thupi la munthu. Kafukufukuyu adzatithandiza kudziwa ngati asilikali angathe kuteteza anthu kuti asatenge HIV.

VRC01 / HIV Virus Attachment from HIV Vaccine Trials Network on Vimeo.

AKUCHITA KAFUKUFUKUYU NDANI?

Kafukufukuyu akuchitika ndi magulu awiri bungwe la HIV Vaccine Trials Network (HVTN) ndi abungwe la HIV Prevention Trials Network (HPTN). Mabungwe awiriwa kuphatikizapo zipatala zonse zimene zikuchita nawo kafukufukuyu adzaonetsetsa kuti kafukufukuyu ndiwovomerezeka kwa amnthu am’deralo dipo adzatsatira zikhalidwe komanso miyambo ya anthu am’maderawo