KUDZIPEREKA KUCHITA NAWO KAFUKUFUKUYU

ZOMWE MUYENERA KUYEMBEKEZERA MUKAGANIZA ZOCHITA NAWO KAFUKUFUKUYU

Tidzakuyankhani mafunso ena alionse amene mungakhale nawo pofuna kuonetsetsa kuti mwamvetsetsa zomwe zimachitika mukalowa nawo m’kafukufukuyu.

  • Tidzawunika thupi lanu kuphatikizapo kuyeza magazi.
  • Panthawi yonse imene mudzakhale mukuchita nawo kafukfukuyu mudzayikidwa madilipi 10, kamodzi pa sabata 8 zilizonse. Kuyika dilipi kumatenga mphindi za pakati pa 30 ndi 60. Mudilipi mumakhala mankhwala a katemera kapena katemera wopanda mankhwala placebo),
  • Tidzakupemphani kuti muzidziona momwe mkukumvera m’thupi mwanu kwa masiku atatu mutalandira katemera. Ogwira ntchito pachipayala cha kafukufuku azidzakufunsani kuti adziwe momwe mukupezera panthawiyi. 
  • Pamaulendo ena otsatira opita kuchipatala mudzakalandira uphungu ndi kuyezetsa HIV, kuyankha mafunso ochokera kwa achipatala. Maulendo amenewa adzakhala achidule kusiyana ndi maulendo amene muzikalandira dilipi ya katemera.