KAFUKUFUKU WOFUFUZA ZA ASILIKALI OTETEZA HIV KUDZERA (AMP HIV PREVENTION STUDY)

Akatswiri a akafukufuku a AMP alengeza zotsatira zoyambirira za akafukufuku a AMP


Mawu akuti AMP ndi achingerezi ndipo amatanthauza Kuteteza HIV Kudzera mwa Asilikali kapena kuti Antibody Mediated Prevention pa Chingerezi. 

Iyi ndi njira yopatsira anthu asilikali pofuna kuona ngati angateteze anthuwo ku kachirombo ka HIV. Kafukufuku wa katemera wa AMP yemwenso amadziwika ndi mayina akuti HVTN 703/HPTN 081 ndi njira yatsopano yotetezera kachirombo ka HIV. Mukafukufuku woyambilira wa HIV, anthu ankalandira katemera ndipo ofufuza amadikira kuti awone ngati matupi a anthuwo angapange chitetezo chogonjetsa kachirombo ka HIV. M’kafukufuku uno, tidumpha ndondomeko imeneyi, ndipo tipereka mankhwalawa kwa powabayira m’misempha pogwiritsa ntchito njira yodziwika kwambiri yoika dilipi. Uyu ndi kafukufuku woyamba wowona ngati chitetezo cha m’thupi chingathe kuteteza kachirombo ka HIV.