Kafukufukuyu akuyembekezera kulemba anthu ochita nawo m’chaka cha 2016 ndipo adzachitikira m’malo awa ku Africa:
Kafukufuku wina wa AMP wofanana ndi uyu akuchitikira m’dziko la America ndi ku South America. Adzayambanso kulembera anthu ochita nawo kafukufukuyu m’chaka cha 2016. Kafukufuku ameneyu akutchedwa HVTN 704/HPTN 085.
Bungwe lowona za matenda a ziwengo komanso matenda opatsirana la National Institute of Allergy and Infectious Diseases (NIAID) lomwe ndi nthambi ya mabungwe a zaumoyo la National Institutes of Health (NIH) ndi amene anapereka ndalama zochitira kafukufukuyu. Bungwe la NIAID pamodzi ndi ndi Gulu la mabungwe oyeserera katemera la HIV Vaccine Trials Network (HVTN) ndi Gulu la mabungwe ochita kaufukufuku woteteza HIV la HIV Prevention Trials Network (HPTN) ndi amene anakonza kafukufukuyu. Bungwe la lofufuza za katemera la Dale and Betty Bumpers Vaccine Research Centre (VCR) lomwe ndi gawo la NIAID ndi lomwe likupereka asilikali a VRC01 mu kafukufukuyu.
Mabungwe a HVTN ndi HPTN ndi mgwirizano wa akatswiri a sayansi, akatswiri a maphunziro komanso anthu wamba amene akusakasaka katemera wabwino wotetezera HIV. Bungwe la HVTN limayang’ana kwambiri za ndondomeko zothandiza kuti katemera wa HIV akhale wosayambitsa zovuta komanso akhale wothandiza pamene bungwe la HPTN limayang’ana za njira zopewera matenda monga kulandira mankhwala oteteza HIV usanakhudzane nayo. A HVTN amalandira thandizo la ndalama kuchokera ku NIAID. A HPTN amalandira thandizo kuchokera NIAID komanso Bungwe la boma la America pantchito yolimbana ndi mankhwala ozunguza ubongo (National Institute on Drug Abuse (NIDA)) kuphatikizapo Bungwe loona za Matenda a Misala la National Institute of mental Health (NIMH).
Cholinga cha akafukufuku onse a mabungwe a HVTN ndi HPTN ndikupeza njira zothandiza kwambiri zotetezera kutenga HIV. Zolinga zenizeni za kafukufukuyu ndi:
Kafukufuku wa HVTN 703/HPTN 081 AMP amayeza asilikali ongoyeserera olimbana ndi HIV mwa amayi opezeka m’mayiko a kunsi kwa chipululu cha Sahara. Mawu akuti AMP ndi achingerezi ndipo amatanthauza Kuteteza HIV pogwiritsa ntchito asilikali ochita kupanga kapena kuti Antibody Mediated Prevention pa Chingelezi. Iyi ndi njira yopatsira anthu asilikali pofuna kuona ngati angateteze anthuwo ku kachirombo ka HIV.
Asilikali am’thupi ndi njira yachilengedwe imene matupi athu amagwiritsa ntchito polimbana ndi matenda. Kupatsa anthu asilikali m’thupi mwawo kuti ateteze matenda ndi njira yovomerezeka pa ntchito zachipatala ndipo njirayi yakhala ikugwira ntchito kwa zoposa 100. Mwachitsanzo, madotolo amapatsa anthu asilikali a m’thupi kuti awateteze ku matenda monga mauka (hepatitis A ndi B) komanso katsabola (chicken pox). Ena mwa asilikali am’thupiwa amagwiritsidwa ntchito poteteza matendawa amapangidwa ndi akatsiwri mu labu. Ena mwa asilikali ochita kupangidwa akhala akugwiritsidwa ntchito bwinobwino poteteza matenda oopsa kwambiri okhudza kupuma mwa ana amene amatchedwa RSV.
Kafukufuku wa katemera wa AMP amayeza katemera wa asilikali otchedwa VRC01 amene amapangidwa mulabu kuti alimbane ndi kachirombo ka HIV. Iyi ndi njira yatsopano yotetezera kachirombo ka HIV yomwe ndiyofanana ndi zomwe zakhala zikuchitika mu kafukufuku wa katemera wa HIV. Mukafukufuku wambiri wa katemera wa HIV, anthu amalandira katemera ndipo ofufuza amadikira kuti awone ngati matupi a anthuwo angapange chitetezo chogonjetsa kachirombo ka HIV. M’kafukufuku uno, tidumpha ndondomeko imeneyi, ndipo tipereka mankhwalawa powabayira m’misempha.
Malinga ndikuwunika kwa mulabu kwasonyeza kuti katemera wa asilikali a VRC01 ameteteza kutenga mitundu yosiyanasiyana ya kachirombo ka HIV. Katemera wa VRC01 anathandizanso kuteteza nyama kutenga matenda. Kafukufuku wa AMP adzatithandizanso kudziwa ngati katemera wa VRC01 angateteze anthu kuti asatenge HIV.
Asilikali a VRC01 anapezeka m’magazi a munthu amene anali ndi HIV ndipo thupi lake linakwanitsa kulimbana ndi HIV kwa zaka 15 popanda kumwa mankhwala a ARV. Katemera wa asilikali a VRC01 sanapangidwe kuchokera HIV yamoyo, HIV yakufa kapena kuthupi la munthu amene ali ndi HIV. Sangayambitse HIV kapena matenda a Edzi. Asilikaliwa anapangidwa mulabu pogwiritsa ntchito dongosolo limene limatsatidwa popanga mankhwala ena onse
Katemera wa VRC01 amaperekedwa kudzera mu dilipi ndipo dilipiyi imayikidwa kwa mphindi za pakati pa 15 ndi 60.Timagwiritsa ntchito singano wotetezedwa pobaya ndi kuyika kachubu kakang’ono mumsempha wa munthuyo. Thumba la madzi limakolekedwa pa chitsulo choyimirira ndikulumikiza ku pampu yomwe imathandiza kuongolera kayendedwe ka madzi a m’thumbawo podutsa m’kachubu kupita mumkono wa munthu wopatsidwayo.
Padzakhala magulu atatu ochuluka mofanana m’kafukufukuyu. Gulu loyamba lidzalandira katemera wa mankhwala ochuluka. Gulu lachiwiri lidzalandira katemera wa mankwhala ochepa.
Gulu lachitatu lidzalandira katemera wopanda mankhwala (placebo).
Mu kafukufukuyu tidzalowetsamo ndikulondoloza amayi okwana pafupifupi 1900 m’malo osiyanasiyana mu Africa.
Amayi am’mayiko a kunsi kwa chipululu cha Sahara ali m’gulu la anthu amene ali pa chiopsezo chachikulu chotenga HIV. Ndiofunikira kuwapezera njira zopewera kutenga kachiromboka kotero kuti ndikofunikira kuti iwo akhale nawo mukafukufuku wofufuza njira zotetezera kutenga kachiromboka.
Kuti mayi alowe nawo m’kafukufukuyu ayenera kukhala wathanzi, wa zaka za pakati pa 18 ndi 40 ndipo kuti alibe HIV. Sangatenge pakati komanso asakhale kuti akuyamwitsa mwana. Komanso pali njira zina zosankhira. Tidzafunsa anthu za mbiri ya umoyo wawo, kuwawunika ndikutenga magazi komanso mkodzo kuti tikayeze. Tidzawafunsanso anthu onse za moyo wawo wogonana komanso ngati amagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo.
Sitikudziwa zoopsa zonse za katemera wa VRC01 chifukwa anangoperekedwako kwa anthu 140 okha m’mbuyomu. Ngakhale kuti palibe amene anakumana ndi vuto lina lililonse lodetsa nkhawa pa kafukufuku wa m’mbuyomu, n’kutheka kuti patha kupezeka zovuta zina zomwe sitimaziyembekezera.
Ichi ndi chifukwa chake cholinga cha kafukufukuyu ndikufuna kudziwa ngati katemerayu sangabweretse zovuta kwa anthu ngati ataperekedwa pamodzi. Tidzakhala tikuyang’anira umoyo wa munthu aliyense amene akuchita nawo kafukufukuyu.
Sitikudziwa. Kafukufuku wa AMP ndi woyamba pa ntchito yofufuza ngati asilikali a VRC01 angateteze kutenga HIV. Ochita nawo kafukufukuyu asaganize kuti angatetezedwe ku HIV chifukwa chochita nawo kafukufukuyu. Choyenera kudziwa ndi chakuti anthu ena ena adzalandira madzi amchere chabe opanda mankhwala (placebo).
Anthu onse ochita nawo kafukufuku adzalandira uphungu wokhudza momwe angapewere makhalidwe amene angachititse kuti atenge HIV.
Popereka uphungu wa kapewedwe ka HIV, anthu ochita nawo kafukufuku ndi aphungu adzakambirana za zinthu monga makondomu, kumwa mankhwala othandiza kupewa kutenga HIV ukhakhudzidwa ndi HIV, kusaledzera ndi kusagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo panthawi yogonana, kuchepetsa chiwerengero cha anthu ogonana nawo ndikukambirana ndi amene mukufuna kukhala nawo paubwenzi ngati wina ali ndi HIV kapena ayi. Aphunguwa angathenso kuwalangiza anthuwa za komwe angakapeze chithandizo cha mankhwala othandiza kupewa kutenga HIV m’deralo ngati atakhudzana nayo munjira zina.
Kasankhidwe ka anthu olowa m’kafukufukuyu nkochitira mayere, kosaona nkhope. Izi zikutanthauza kuti kaya munthu alandira katemera wa mankhwala ochuluka kapena ochepa kapena placebo izi zidzachitika mosachita kusankha ngati momwe timachitira mayere oponya khobidi m’mwamba. Cholinga cha kusankha kotere ndi chakuti m’magulu atatu aja mukhale anthu ochuluka mofanana. Anthu onse a m’maguluwa adzalandira uphungu wofanana pakapewedwe ka HIV, choncho kuopsa kwa HIV ndikofanana kwa magulu onse. Tikudziwa kuti ngakhale titayesetsa kuphunzitsa anthu za kupewa kutenga HIV, anthu ena adzatengabe HIV. Kusiyana kwakulu m’maguluwa ndi kwakuti ena adzalandira katemera wa mankhwala pamene ena adzalandira katemera wopanda mankhwala (placebo). Choncho chifukwa chakuti china chilichonse m’maguluwa ndichofanana, kusiyana kumene kungapezeke ndiye kuti kudzachitika chifukwa cha katemerayu (asilikaliwa).
Tikuyembekezea kuti kafukufukuyu adzatenga zaka 5 kuti athe. Munthu aliyense wochita nawo kafukufukuyu adzakhala nawo m’kafukufukuyu kwa zaka zosachepera ziwiri.
Pakadali pano palibe chikonzero chopereka katemerayu kwa anthu ochita nawo kafukufukuyu ntchitoyi ikadzatha kapena kupeza chilolezo choti anthu ena azigwiritsa ntchito. M’malo mwake tidzagwiritsa ntchito zomwe tidzapeze m’kafukufukuyu pochita izi:
Ayi, sitikuyembekezera kuti zingatheke kuti munthu aoneke ngati ali ndi HIV atayezetsa pamene alibe. Takhala tikuyeza kambirimbiri magazi a anthu omwe ali ndi VRC01 pogwiritsa ntchito njira zoyezera HIV kuti tione ngati VRC01 angachititse kuti munthu amene alibe HIV azioneka ngati ali nayo. Poyeza mulabu zimenezi sizinachitike. Tikuyezabe kuti tikhale ndi chitsimikizo cha zotsatira zimenezi.
Kuteteza umoyo ndi kulemekeza ufulu wa anthu ochita nawo kafukufuku ndi zinthu zimene timaziyikira kumtima kwambri pochita kafukufuku wa HVTN ndi HPTN. Sitingathe kupeza njira zatsopano zotetezera HIV popanda anthu odzipereka kuchita nawo kafukufukuyu
Njira yoyamba pofuna kuteteza anthu ochita nawo kafukufuku ndikuwafotokozera zonse zokhudza kafukufukuyu asanalowe. Izi zimathandiza kuti ochita nawo kafukufuku avomereze atadziwa zomwe zikuchitika. Ogwira ntchito mu zipatala za kafukufukuyu adzafotokozera anthu za katemerayu, dongosolo loyenera kutsata mu kafukufukuyu, kuopsa kwake komanso ubwino wake kwa iwowo komanso za ufulu umene iwo ali nawo. Izi ndi monga kudziwitsidwa nkhani zatsopano zokhudza kafukufukuyu makamaka zinthu zimene zingawathandize posankha kulowa nawo, komanso za ufulu wotuluka mu kafukufukuyu nthawi ina iliyonse.
Panthawi ya kafukufukuyu, ogwira ntchito pachipatalapo adzayang’anira anthu ochita nawo kafukufuku pofuna kuonetsetsa kuti katemerayu sakuyambitsa zovuta zina pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Ogwira ntchito za kafukufukuku adzafunsa anthuwa ngati akukumana ndi zovuta za pamoyo wawo chifukwa chochita nawo kafukufukuyu. Ngati wochita nawo kafukufuku ali ndi vuto la zaumoyo kapena moyo wake wa tsiku ndi tsiku limene layamba chifukwa chochita nawo kafukufukuyu, achipatala adzawathandiza.
Palinso magulu angapo amene amagwira ntchito yoteteza ufulu ndi umoyo wa anthu amene akuchita nawo kafukufuku:
Za kafukufuku wa AMP: www.ampstudy.org.za
Za mabungwe amene akuchita kafukufuku woyeserera katemera wa HIV: www.hvtn.org
Za mabungwe amene akuchita kafukufuku woyeserera njira zopewera HIV: www.hptn.org
Ngati muli ndi mafunso ena amene sitinathe kuwayankha pakufotokoza kwathuku, chonde tifunseni. Mutha kuyankhulana ndi: [email protected]