Akafukufuku anasonyeza kuti asilikali am’thupi opangidwa mu labu amene amagonjetseratu HIV a VRC01 atha kuteteza kutenga mitundu ina ya HIV popanda kubweretsa vuto lina lililonse. 

  • Koma, mankhwala a AMP VRC01 sanakwanitse mokwanira kutetezeratu kutenga HIV.
  • Izi zikutanthauza kuti tidzayenera kugwiritsa ntchito mintundu ingapo ya asilikali am’thupi kuti tithe kuteteza kutenga HIV pogwiritsa ntchito asilikali am’thupi ochita kupanga mu labu..

Akafukufuku a AMP anakhazikitsidwa m’madera onse m’mwezi wa October, 2018. Akafukufuku awiri a Gulu 2b amene akuyendetsedwa ndi bungwe la HIV Vaccine Trials Network (HVTN) ndi bungwe la HIV Prevention Trials Network (HPTN) analemba anthu okwana 4,625 pamene anali pachiopsezo chotenga HIV m’mayiko a Kumpoto ndi Kumwera kwa America, ku Europe, ndi Kumwera kwa Africa.

Akafukufukuwa akupitirirabe ndipo sitiulula mankhwala amene anthu otenga nawo mbali analandira mpaka anthu onse atamaliza maulendo awo otsiriza opita kuchipatala, amene akuyembekezeka kudzachitika kumayambiriro kwa 2021.

Zambiri za akafukufuku a AMP ndi zotsatira zake zikupezeka pano: